Bukhu latsopanoli, “Luso la Utumiki” ndi lofunika kwambiri kwa onse amene amakhumbira kuchita ntchito ya Mulungu. Limawonetseratu maganizo omwe ali olondola ndi oipa okhudzana ndi utumiki, chomwe ntchito ya utumiki chiri, chomwe mukuyenera kuchita ngati wogwira ntchito mu utumiki ndi momwe mungapangire ntchito za mtumiki.
Mwadabwapo zokhuzana ndi momwe mungachitire ntchito ya utumiki? Bukhu lapaderali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills likakulimbikitsani inu kuyenda moyenereza maitanidwe an a Mulungu ndi kukutsogozani inu mu kudzipereka nokha kwathunthu ku ntchito ya Mulungu.