Azibusa ali pa mpani pani wokondweretsa ndi kusangalatsa anthu awo ndi uthenga wabwino. Mpani pani wa anthu umenewu wapangitsa kusintha kwa mawu a Khristu kufikira mawu a mtanda akhalira kovuta kuzindikirika.Lero, tikubwerera ku maziko a chilungamo cha Chikhristu choti tikuyenera “kutaya” kuti “tipeze” Khristu. Mphamvu izabwerera ku mpingo pamene tikulalikira kuti tipereke nsembe, kusautsidwa ndi kufa chifukwa cha Khristu. Mphamvu ya mawu a Khristu siingafufutidwe ndi wina aliyense posatengera kuchita bwino kapena kukhala wa mphamvu.